Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 20:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Nati Yesaya, Cizindikilo ndici akupatsa Yehova, kuti Yehova adzacicita conena iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi?

10. Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.

11. Napfuulirakwa Yehova Yesayamneneriyo, nabweza iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.

12. Nthawi ija Berodaki Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Sabulo anatumiza akalata ndi mtulo kwa Hezekiya, popeza adamva kuti adadwala Hezekiya.

13. Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya cuma cace, siliva, ndi golidi, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zace, ndi zonse zopezeka pacuma pace; panalibe kanthu m'nyumba mwace, kapena m'ufumu wace wonse osawaonetsa Hezekiya.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 20