Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 2:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo kunali ataoloka, Eliya anati kwa Elisa, Tapempha cimene ndikucitire ndisanacotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, Mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine.

10. Nati iye, Wapempha cinthu capatali, koma ukandipenya pamene ndicotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero at.

11. Ndipo kunacidka, akali ciyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka gareta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kabvumvulu.

12. Ndipo Elisa anapenya, napfuula, Atate wanga, atate wanga, gareta wa Israyeli ndi apakavalo ace! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zobvala zace zace, nazing'amba pakati.

13. Pamenepo anatola copfunda cace ca Eliya cidamtayikiraco, nabwerera, naima m'mphepete mwa Yordano.

14. Ndipo anatenga copfunda ca Eliya cidamtayikiraco, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 2