Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 19:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, atamva Hezekiya, anang'amba zobvala zace, napfundira ciguduli, nalowa m'nyumba ya Yehova.

2. Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akuru a ansembe opfundira ciguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi.

3. Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero line ndilo tsiku la cisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.

4. Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asuri mbuye wace, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga cifukwa ca mau adawamva Yehova Mulungu wanu; cifukwa cace uwakwezere otsalawo pemphero.

5. Ndipo anyamata a mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.

6. Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asuri anandicitira nao mwano.

7. Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kumka ku dziko lace, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lace.

8. Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asuri alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adacoka ku Lakisi.

9. Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, waturuka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,

10. Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asuri.

11. Taona, udamva ico mafumu a Asuri anacitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi?

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 19