Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 18:25-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ngati ndakwerera malo ana wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga.

26. Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yoa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Ciaramu; popeza ticimva ici; musalankhule nafe m'Ciyuda, comveka ndi anthu okhala palinga.

27. Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?

28. Naima kazembeyo, napfuula ndi mau akulu m'Ciyuda, nanena kuti, Tamverani mau a mfumu yaikuru mfumu ya Asuri.

29. Itero mfumu, Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m'dzanja lace;

30. kapena Hezekiya asakukhulupiritseni pa Yehova, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa ndithu, ndi mudzi uwu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asuri.

31. Musamvere Hezekiya; pakuti Itero mfumu ya Asuri, Mupangane nane zamtendere, nimuturukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wace, ndi yense ku mkuyu wace, ndi kumwa yense madzi a m'citsime cace;

32. mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uci; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.

33. Kodi mlungu uli wonse wa amitundu walanditsa dziko lace m'dzanja la mfumu ya Asuri ndi kale lonse?

34. Iri kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa?

35. Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?

36. Koma anthuwo anakhala cete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 18