Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 18:22-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamcotsera misanje yace ndi maguwa a nsembe ace, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira pa guwa la nsembe pane m'Yerusalemu?

23. Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.

24. Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata ang'ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Aigupto akupatse magareta ndi apakavalo?

25. Ngati ndakwerera malo ana wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga.

26. Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yoa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Ciaramu; popeza ticimva ici; musalankhule nafe m'Ciyuda, comveka ndi anthu okhala palinga.

27. Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?

28. Naima kazembeyo, napfuula ndi mau akulu m'Ciyuda, nanena kuti, Tamverani mau a mfumu yaikuru mfumu ya Asuri.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 18