Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 18:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cacitatu ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu waceo

2. Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Abi mwana wa Zekariya.

3. Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita Davide kholo lace.

4. Anacotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha cifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israyeli anaifukizira zonunkhira, naicha Cimkuwa.

5. Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israyeli; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.

6. Pakuti anaumirira Yehova osapambuka pambuyo pace, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.

7. Ndipo Yehova anali naye, nacita iye mwanzeru kuli konse anamukako, napandukira mfumu ya Asuri osamtumikira.

8. Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ace, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mudzi walinga.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 18