Anacotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha cifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israyeli anaifukizira zonunkhira, naicha Cimkuwa.