Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 17:3-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asuri kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.

4. Koma mfumu ya Asuri anampeza Hoseya alikucita ciwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Aigupto, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asuri, monga akacita caka ndi caka; cifukwa cace mfumu ya Asuri anamtsekera, nammanga m'kaidi.

5. Pamenepo mfumu ya Asuri anakwera m'dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu.

6. Caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Asuri analanda Samariya, natenga Aisrayeli andende, kumka nao ku Asuri; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi.

7. Kudatero, popeza ana a Israyeli adacimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwaturutsa m'dziko la Aigupto pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, ndipo anaopa milungu yina,

8. nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli, ndi m'miyambo ya mafumu a Israyeli imene iwo anawalangiza.

9. Ndipo ana a Israyeli anacita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse ku nsanja ya olonda ndi ku mudzi walinga komwe.

10. Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa citunda ciri conse cacitali, ndi patsinde pa mtengo uli wonse wogudira;

11. nafukizapo zonunkhira pa misanje youse, monga umo amacitira amitundu amene Yehova adawacotsa pamaso pao, nacita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;

12. natumikira mafano amene Yehova anawanena nao, Musacita ici.

13. Ndipo Yehova anacitira umboni Israyeli ndi Yuda mwa dzanja la mneneri ali yense, ndi mlauli ali yense, ndi kuti, Bwererani kuleka nchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa cilamulo conse ndinacilamulira makolo anu, ndi kucitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.

14. Koma sanamvera, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirira Yehova Mulungu wao.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 17