Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 16:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napitikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komweko kufikira lero lino.

7. Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israyeli anandiukirawo.

8. Natenga Ahazi siliva ndi golidi wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asuri.

9. Nimmvera mfumu ya Asuri, nikwera kumka ku Damasiko mfumu ya Asuri, niulanda, nipita nao anthu ace andende ku Kiri, nimupha Rezini.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 16