Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 16:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe cithunzithunzi cace, ndi cifanizo cace, monga mwa mamangidwe ace onse.

11. Ndipo Uriya wansembe anamanga guwa la nsembelo, monga mwa zonse anazitumiza mfumu Ahazi zocokera ku Damasiko; momwemo Uriya wansembe analimanga asanabwere mfumu ku Damasiko.

12. Atafika mfumu kucokera ku Damasiko, anapenya mfumu guwa la nsembelo, nayandikiza mfumu ku guwa la nsembelo, napereka nsembe pomwepo.

13. Nafukiza nsembe yace yopsereza ndi nsemba yace yaufa, natsanulira nsembe yace yothira, nawaza mwazi wa nsembe zace zamtendere pa guwa la nsembelo,

14. Nalicotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamasopa Yehova, nalicotsa kukhomo la nyumba pakati pa guwa la nsembe lace ndi nyumba ya Yehova, naliikakumpotokwa guwa la nsembe lace.

15. Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Pa guwa la nsembe lalikuru uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yace yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.

16. Nacita Uriya wansembe monga mwa zonse adalamulira mfumu Ahazi.

17. Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nacotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng'ombe zamkuwa ziri pansi pace, naziika pa ciunda camiyala.

18. Nacotsa ku nyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, cifukwa ca mfumu ya Asuri.

19. Macitidwe ena tsono adawacita Ahazi, salembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

20. Nagona Ahazi ndi makolo ace, namuika ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwace Hezekiya mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 16