Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 15:4-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Komatu sanaicotsa misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

5. Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yace, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.

6. Macitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

7. Nagona Azariya ndi makolo ace, namuika ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwace Yotamu mwana wace.

8. Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobiamu anakhala mfumu ya Israyeli m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi.

9. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga adacita makolo ace; sanaleka zolakwa zace za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.

10. Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamcitira ciwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.

11. Macitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

12. Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli. Ndipo kunatero momwemo.

13. Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wace caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai ca Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi m'Samariya.

14. Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kucokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi m'Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.

15. Macitidwe ena tsono a Salumu ndi ciwembu cace anacicita, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 15