Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 14:15-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Macitidwe ena tsono a Yoasi adazicita, ndi mphamvu yace, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

16. Nagona Yoasi ndi makolo ace, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israyeli; nakhala mfumu m'malo mwace Yerobiamu mwana wace.

17. Ndipo Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yoasi mwana wa Yoahazi mfumu ya Israyeli, zaka khumi ndi zisanu.

18. Macitidwe ena tsono a Amaziya, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

19. Ndipo anamcitira ciwembu m'Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.

20. Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide.

21. Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace Amaziya,

22. Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, atagona ndi makolo ace mfumuyo.

23. Caka cakhumi ndi zisanu ca Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda, Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli analowa ufumu wace m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu cimodzi.

24. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, sanaleka zolakwa zonse za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.

25. Anabweza malire a Israyeli kuyambira polowera ku Hamati mpaka nyanja ya kucidikha, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israyeli, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wace Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gati-heferi,

26. Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israyeli nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israyeli.

27. Ndipo Yehova sadanena kuti adzafafaniza dzina la Israyeli pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobiamu mwana wa Yoasi.

28. Macitidwe ena tsono a Yerobiamu, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace, umo anacita nkhondo, nabweza kwa Israyeli Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

29. Ndipo Yerobiamu anagona ndi makolo ace, ndiwo mafumu a Israyeli; nakhala mfumu m'malo mwace Zekariya mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 14