Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 13:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israyeli, nawapereka m'dzanja la Hazaeli mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaeli, masiku onsewoo

4. Koma Yoahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwace kwa Israyeli m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.

5. Ndipo Yehova anapatsa Israyeli mpulumutsi, naturuka iwo pansi pa dzanja la Aaramu; nakhala ana a Israyeli m'mahema mwao monga kale.

6. Komatu sanalekana nazo zolakwa za nyumba ya Yerobiamu, zimene analakwitsa nazo Israyeli, nayenda m'mwemo; nicitsalanso cifanizo m'Samariya.

7. Koma mfumu ya Aramu sanasiyira Yoahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magareta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati pfumbi lopondapo.

8. Macitidwe ena tsono a Yoahazi, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

9. Ndipo Yoahazi anagona ndi makolo ace, namuika m'Samariya; nakhala mfumu m'malo mwace Yoasi mwana wace.

10. Caka ca makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri ca Yoasi mfumu ya Yuda, Yoasi mwana wa Yoahazi analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi.

11. Nacita coipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli, koma anayendamo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 13