Koma Yoahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwace kwa Israyeli m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.