Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 13:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Caka ca makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri ca Yoasi mfumu ya Yuda, Yoasi mwana wa Yoahazi analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi.

11. Nacita coipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli, koma anayendamo.

12. Macitidwe ena tsono a Yoasi, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace yocita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

13. Ndipo Yoasi anagona ndi makolo ace, ndi Yerobiamu anakhala pa mpando wacifumu wace; namuika Yoasi m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israyeli.

14. Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yoasi mfumu ya Israyeli, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, gareta wa Israyeli ndi apakavalo ace!

15. Nanena naye Elisa, Tenga uta ndi mibvi; nadzitengera uta ndi mibvi.

16. Nati kwa mfumu ya Israyeli, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ace pa manja a mfumu.

17. Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Mubvi wa cipulumutso wa Yehova ndiwo mubvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m'Afeki mpaka mudzawatha.

18. Nati iye, Tengani mibvi; naitenga, Nati kwa mfumu ya Israyeli, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.

19. Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.

20. Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amoabu analowa m'dziko poyambira caka.

21. Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima ciriri.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 13