Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 12:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo pakuona kuti ndarama zidacuruka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkuru wansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.

11. Napereka ndarama zoyesedwa m'manja mwa iwo akucita nchitoyi, akuyang'anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira nchito ya pa nyumba ya Yehova,

12. ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.

13. Koma sanapangira nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera ziri zonse zagolidi, kapena zotengera ziri zonse zasiliva, kuzipanga ndi ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Yehova;

14. pakuti anazipereka kwa iwo akugwira nchitoyi, nakonza nazo nyumba ya Yehova.

15. Ndipo sanawerengera anthu, amene anapereka ndaramazi m'manja mwao kuti apatse ogwira nchito; popeza anacita mokhulupirika.

16. Ndarama za nsembe zoparamula ndi ndarama za nsembe yaucimo sanabwera nazo ku nyumba ya Yehova; nza ansembe izi.

17. Pamenepo Hazaeli mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yace kukwera ku Yerusalemu.

18. Koma Yoasi mfumu ya Yuda: anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yoramu, ndi Ahaziya, makolo ace, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zace zace, ndi golidi yense anampeza pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi ca nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaeli mfumu ya Aramu; motero anabwerera kucoka ku Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 12