Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 11:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo atsogoleri a mazana anacita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ace olowera pa Sabata, ndi oturukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.

10. Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova.

11. Ndipo otumikira anakhala ciriri yense ndi zida zace m'manja mwace, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

12. Atatero, anaturutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfomu ikhale ndi movo.

13. Pamene Ataliya anamva phokoso la otumikira ndi anthu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova;

14. napenya, ndipo taonani, mfumu iri ciriri paciundo, monga adafocita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfomu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zobvala zace, napfuula, Ciwembu, Ciwembu.

15. Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumturutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova.

16. Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo ku nyumba ya mfumu, namupha pomwepo.

17. Ndipo Yehoyada anacita cipangano pakati pa Yehova ndi mfomu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 11