Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 11:2-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Koma Yoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wace wa Ahaziya, anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'cipinda cogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwa.

3. Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi cimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.

4. Koma caka cacisanu ndi ciwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye ku nyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.

5. Nawalamulira, kuti, Cocita inu ndi ici: limodzi la magawo atatu la inu olowa pa Sabata lizilindira nyumba ya mfumu,

6. ndi lina lizikhala ku cipata ca Suri, ndi lina ku cipata kumbuyo kwa otumikira; momwemo muzisunga nyumba, ndi kuicinjiriza.

7. Ndipo magawo awiri ainu, ndiwo onse oturukira pa Sabata, azilindira nyumba ya Yehova kuzinga mfumu.

8. Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zace m'manja mwace, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu poturuka ndi polowa iye.

9. Ndipo atsogoleri a mazana anacita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ace olowera pa Sabata, ndi oturukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.

10. Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova.

11. Ndipo otumikira anakhala ciriri yense ndi zida zace m'manja mwace, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 11