Koma Yoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wace wa Ahaziya, anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'cipinda cogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwa.