Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 11:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo otumikira anakhala ciriri yense ndi zida zace m'manja mwace, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

12. Atatero, anaturutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfomu ikhale ndi movo.

13. Pamene Ataliya anamva phokoso la otumikira ndi anthu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova;

14. napenya, ndipo taonani, mfumu iri ciriri paciundo, monga adafocita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfomu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zobvala zace, napfuula, Ciwembu, Ciwembu.

15. Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumturutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova.

16. Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo ku nyumba ya mfumu, namupha pomwepo.

17. Ndipo Yehoyada anacita cipangano pakati pa Yehova ndi mfomu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.

18. Namuka anthu onse a m'dzikomo ku nyumba ya Baala, naigumula; maguwa ace a nsembe ndi mafano ace anawaswaiswa, napha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova.

19. Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m'dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu ku nyumba ya Yehova, nadzera njira ya cipata ca otumikira, kumka ku nyumba ya mfomu. Nakhala Iye pa cimpando ca mafumu.

20. Nakondwerera anthu onse a m'dziko, ndi m'mudzi munali phe; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga ku nyumba ya mfumu.

21. Yoasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 11