Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 10:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Ahabu anali nao ana amuna makumi asanu ndi awiri m'Samariya. Nalemba akalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezreeli, ndiwo akulu akulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,

2. Tsono akakufikani inu kalata uyu, popeza muli nao ana a mbuye wanu; muli naonso magareta ndi akavalo, ndi mudzi walinga, ndi zida,

3. musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wacifumu wa atate wace; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.

4. Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaima pamaso pace, nanga ife tidzaima bwanji?

5. Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akulu akulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzacita; sitidzalonga munthu yense mfumu; cokomera pamaso panu citani.

6. Nawalembera kalata kaciwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu va amunawo ana a mbuyewanu, ndi kundidzera ku Yezreeli mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 10