Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 8:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pamene Samueli anakalamba, anaika ana ace amuna akhale oweruza a Israyeli.

2. Dzina la mwana wace woyamba ndiye Yoeli, ndi dzina la waciwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba.

3. Ndipo ana ace sanatsanza makhalidwe ace, koma anapambukira ku cisiriro, nalandira cokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.

4. Pamenepo akuru onse a Israyeli anasonkhana, nadza kwa Samueli ku Rama;

5. nanena naye, Taonani, mwakalamba, ndipo ana anu satsanza makhalidwe anu; tsono, mutilongere mfumu kuti ikatiweruze, monga umo mucitidwa m'mitundu yonse ya anthu.

6. Koma cimeneci sicinakondweretsa Samueli, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samueli anapemphera kwa Yehova.

7. Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.

8. Monga nchito zao zonse anazicita kuyambira tsiku lija ndinawaturutsa ku Aigupto, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu yina, momwemo alikutero ndi iwenso.

9. Cifukwa cace tsono umvere mau ao koma uwacenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ace a mfumu imene idzawaweruza.

10. Ndipo Samueli anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova,

11. Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu amuna, akhale akusunga magareta, ndi akavale ace; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magareta ace;

12. idzawaika akhale otsogolera cikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yace, ndi kutema dzinthu zace, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magareta.

13. Ndipo idzatenga ana anu akazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 8