Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 6:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.

2. Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Ticitenji ndi likasa la Yehova? mutidziwitse cimene tilitumize naco kumalo kwace.

3. Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israyeli, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yoparamula, mukatero mudzaciritsidwa, ndi kudziwa cifukwa cace dzanja lace liri pa inu losacoka.

4. Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yoparamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolidi, ndi mbewa zisanu zagolidi, monga mwa ciwerengo ca mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.

5. Cifukwa cace muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo mucitire ulemu Mulungu wa lsrayeli; kuti kapena adzaleza dzanja lace pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi pa dziko lanu.

6. Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aaigupto ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sana lola anthuwo amuke, iye atacita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?

7. Cifukwa cace tsono, tengani, nimukonze gareta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli cikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagareta, muzicotsere ana ao kunka nao kwanu;

8. ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaretapo; nimuike zokometsera zagolidi, zimene muzipereka kwa iye ngati nsembe yoparamula, m'bokosi pam bali pace; nimulitumize licoke.

9. Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire ace ace ku Betisemesi, iye anaticitira coipa ici cacikuru; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, siliri lace; langotigwera tsokali.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 6