Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israyeli, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yoparamula, mukatero mudzaciritsidwa, ndi kudziwa cifukwa cace dzanja lace liri pa inu losacoka.