Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 4:19-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo mpongozi wace, mkazi wa Pinehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yace yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wace, ndi mwamuna wace anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kucira kwace kwamdzera.

20. Ndipo pamene adati amwalire, anthu akazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankha, kapena kusamalira.

21. Ndipo iye anamucha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wacoka kwa Israyeli; cifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi cifukwa ca mpongozi wace ndi mwamuna wace.

22. Ndipo iye anati, Ulemerero wacoka kwa Israyeli; cifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 4