Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 27:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide ananena mumtima mwace, Tsiku tina Sauli adzandipha; palibe cina condikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Sauli adzakhala kakasi cifukwa ca ine, osandifunanso m'malire onse a Israyeli, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lace.

2. Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.

3. Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ace, munthu yense ndi a pabanja pace, inde Davide ndi akazi ace awiri, Ahinoamu wa ku Jezreeli, ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wa Nabala.

4. Ndipo anauza Sauli kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunanso.

5. Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumiraga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wacifumu pamodzi ndi inu?

6. Ndipo Akisi anampatsa Zikilaga tsiku lomweli; cifukwa cace Zikilaga ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.

7. Ndipo kuwerenga kwace kwa masiku Davide anakhala ku dziko la Afilisti ndiko caka cimodzi ndi miyezi inai.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 27