Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 26:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Azifi anafika kwa Sauli ku Gibeya, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hagila, kupenya kucipululu!

2. Ndipo Sauli ananyamuka, natsikira ku cipululu ca Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israyeli osankhika, kukafuna Davide m'cipululu ca Zifi.

3. Sauli namanga zithando m'phiri la Hagila kupenya kucipululu kunjira, Koma Davide anakhala kucipululu, naona kuti Sauli alikumfuna kucipululu komweko.

4. Cifukwa cace Davide anatumiza ozonda, nazindikira kuti Sauli anabwera ndithu,

5. Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo pala Sauli anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Sauli, ndi Abineri mwana wa Neri kazembe wa khamu lace; ndipo Sauli anagona pakati pa linga la magareta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pace.

6. Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Mhiti, ndi Abisai mwana wa Zeruya, mbale wace wa Yoabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Sauli? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.

7. Comweco Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Sauli anagona tulo m'kati mwa linga la magareta, ndi mkondo wace wozika kumutu kwace; ndi Abineri ndi anthuwo anagona pomzinga iye.

8. Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.

9. Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lace pa wodzozedwa wa Mulungu, ndi kukhala wosacimwa?

10. Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yace lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.

11. Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwace, ndi cikho ca madzi, ndipo tiyeni, timuke.

12. Comweco Davide anatenga mkondowo, ndi cikho ca madzi ku mutu wa Sauli nacoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anati m'tulo; popeza tulo tatikuru tocokera kwa Yehova tinawagwira onse.

13. Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba pa phiri; pakati pao panati danga lalikuru;

14. ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abineri mwana wa Neri, nati, Suyankha kodi Abineri? Tsono Abineri anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo?

15. Davide nati kwa Abineri, Si ndiwe mwamuna weni weni kodi? ndani mwa Aisrayeli afanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 26