Comweco Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Sauli anagona tulo m'kati mwa linga la magareta, ndi mkondo wace wozika kumutu kwace; ndi Abineri ndi anthuwo anagona pomzinga iye.