Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Mhiti, ndi Abisai mwana wa Zeruya, mbale wace wa Yoabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Sauli? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.