Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 25:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pomwepo Abigayeli anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoocaoca, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi ncinci za mphesa zouma zana limodzi, ndi ncinci za nkhuyu mazana awiri, naziika pa aburu.

19. Nati kwa anyamataace, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuvo mwanu. Koma sanauza mwamuna wace Nabala.

20. Ndipo kudatero pakuberekeka iye pa buru wace, natsikira pa malo obisika a m'phirilo, onani, Davide ndi anthu ace analikutsikira kwa iye; iye nakomana nao.

21. Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga cabe zace zonse za kaja kanali nazo m'cipululu, sikadasowa kanthu ka zace zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.

22. Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m'mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo.

23. Ndipo Abigayeli pakuona Davide, anafulumira kutsika pa bum, nagwa pamaso pa Davide nkhope yace pansi, namgwadira,

24. Ndipo atagwadira pa mapazi ace anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale ucimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 25