Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 25:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo.

17. Cifukwa cace tsono mudziwe ndi kulingalira cimene mudzacita; popeza anatsimikiza mtima kucitira coipa mbuye wathu, ndi nyumba yace yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.

18. Pomwepo Abigayeli anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoocaoca, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi ncinci za mphesa zouma zana limodzi, ndi ncinci za nkhuyu mazana awiri, naziika pa aburu.

19. Nati kwa anyamataace, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuvo mwanu. Koma sanauza mwamuna wace Nabala.

20. Ndipo kudatero pakuberekeka iye pa buru wace, natsikira pa malo obisika a m'phirilo, onani, Davide ndi anthu ace analikutsikira kwa iye; iye nakomana nao.

21. Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga cabe zace zonse za kaja kanali nazo m'cipululu, sikadasowa kanthu ka zace zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 25