Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 24:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, Sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; cifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.

11. Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe coipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakucimwirani, cinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire,

12. Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu; ndipo Yehova adzandibwezera cilango kwa inu; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.

13. Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Ucimo uturukira mwa ocimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.

14. Nanga mfumu ya Israyeli inaturukira yani; inu mulikupitikitsa yani? Garu wakufa, kapena nsabwe.

15. Cifukwa cace Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, oandigwirire moyo, oandipulumutse m'dzanja lanu.

16. Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Sauli, Sauli anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Sauli nakweza mau ace, nalira misozi.

17. Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.

18. Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandicitira zabwino cifukwa sunandipha pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.

19. Pakuti munthu akapeza mdani wace, adzamleka kodi kuti acoke bwino? Cifukwa cace Yehova akubwezere zabwino pa ici unandicitira ine lero lomwe.

20. Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israyeli udzakhazikika m'dzanja lako.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 24