Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 19:3-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. ndipo ine ndidzaturuka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa.

4. Ndipo Jonatani analankhula ndi atate wace mobvomereza Davide, nanena naye, Mfumu asacimwire mnyamata wace Davide; cifukwa iyeyo sanacimwira inu, ndipo nchito zace anakucitirani zinali zabwino ndithu;

5. popeza iye anataya moyo wace nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anacitira Aisrayeli onse cipulumutso cacikuru, inu munaciona, nimnnakondwera; tsono mudzacimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda cifukwa?

6. Ndipo Sauli anamvera mau a Jonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye.

7. Pamenepo Jonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Jonatani anafika naye Davide kwa Sauli, iye nakhalanso pamaso pace monga kale.

8. Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anaturuka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe akuru, ndipo iwo anamthawa iye.

9. Ndipo mzimu woipa wocokera kwa Yehova unali pa Sauli, pakukhala iye m'nyumba mwace, ndi mkondo wace m'dzanja lace; ndipo Davide anayimba ndi dzanja lace.

10. Ndipo Sauli anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kucoka pamaso pa Sauli; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja.

11. Ndipo Sauli anatumiza mithenga ku nyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.

12. Comweco Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka.

13. Ndipo Mikala anatenga cifanizo naciika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwace, nacipfunda zopfunda.

14. Ndipo pamene Sauli anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, iye alikudwala.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 19