Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 18:25-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Nati Sauli, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna colowolera cina, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere cilango adani a mfumu. Koma Sauli anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.

26. Ndipo pamene anyamata ace anauza Davide mau awa, kudamkomera Davide kukhala mkamwini wa mfumu.

27. Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ace, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Sauli anampatsa Mikala mwana wace wamkazi akhale mkazi wace.

28. Ndipo Sauli anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Sauli anamkonda Davide.

29. Sauli nayamba kumuopa Davide kopambana; ndi Sauli anali mdani wa Davide masiku onse.

30. Pomwepo mafumu a Afilisti anaturuka; ndipo nthawi zonse anaturuka iwo, Davide anali wocenjera koposa anyamata onse a Sauli, comweco dzina lace linatamidwa kwambiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 18