Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 17:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-damimu.

2. Ndipo Sauli ndi anthu a Israyeli anasonkhana, namanga zithando pa cigwa ca Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.

3. Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisrayeli anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali cigwa.

4. Ndipo ku zithando za Afilisti kunaturuka ciwinda, dzina lace Goliate wa ku Gati, kutalika kwace ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi cikhato.

5. Ndipo anali ndi cisoti camkuwa pamutu pace, nabvala maraya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa,

6. nakuta msongolo wace ndi cobvala camkuwa, ndiponso pacikota pace panali nthungo yamkuwa.

7. Ndipo mtengo wa mkondo wace unali ngati mtanda woombera nsaru; ndi khali la mkondowo linalemera ngati masekeli mazana asanu ndi limodzi a citsulo; ndipo womnyamulira cikopa anamtsogolera.

8. Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israyeli, nanena nao, Munaturukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Sauli? mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 17