Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 14:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali tsiku lina kuti Jonatani mwana wa Sauli ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauza atate wace.

2. Ndipo Sauli analikukhala m'matsekerezo a Gibeya patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migroni; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi;

3. ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wace wa Ikabodi, mwana wa Pinehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wobvala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwa kuti Jonatani wacoka.

4. Ndipo pakati pa mipata imene Jonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali yina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzace; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzace ndilo Sene.

5. Phiri lija linaimirira kuyang'ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzace kumwera pandunji pa Geba.

6. Ndipo Jonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira nchito; pakuti palibe comletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.

7. Ndipo wonyamula zida zace ananena naye, Citani zonse ziri mumtima mwanu; palukani, onani ndiri pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.

8. Ndipo Jonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziu lula kwa iwo.

9. Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m'malo mwathu, osakwera kwa iwo.

10. Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ici cidzatikhalira cizindikilo.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 14