Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 12:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Samueli anauza Aisrayeli onse, kuti, Onani dani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu.

2. Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga amuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.

3. Ndikalipo ine; citani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wace; ndinalanda ng'ombe ya yani? kapena ndinalanda buru wa yani? ndinanyenga yani? ndinasautsa yani? ndinalandira m'manja mwa yani cokometsera mlandu kutseka naco maso anga? ngati ndinatero ndidzacibwezera kwa inu.

4. Ndipo iwo anati, Simunatinyenga, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina ali yense.

5. Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wace ali mboni lero kuti simunapeza kanthu m'dzanja langa, Nati iwo, iye ali mboni.

6. Ndipo Samueli ananena ndi anthuwo, Yehova ndiye amene anaika Mose ndi Aroni, naturutsanso makolo anu m'dziko la Aigupto,

7. Cifukwa cace tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova za nchito zonse zolungama za Yehova, anakucitirani inu ndi makolo anu.

8. Pamene Yakobo anafika ku Aigupto, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anaturutsa makolo anu m'Aigupto, nawakhalitsa pamalo pano,

9. Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Moabu, iwo naponyana nao.

10. Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinacimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu.

11. Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Bedani, ndi Yefita, ndi Samueli, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.

12. Ndipo pamene munaona kuti Nahasi mfumu ya ana a Amoni inadza kuponyana nanu, munanena ndi ine, Koma mfumu itiweruze; ngakhale mfumu yanu ndiye Yehova Mulungu wanu.

13. Cifukwa cace siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 12