Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 11:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Nahasi M-amoni anakwera, namanga Yabezi Gileadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabezi anati kwa Nahasi, Mupangane cipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu.

2. Ndipo Nahasi Mamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisrayeli onse.

3. Ndipo akuru a ku Yabezi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israyeli; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzaturukira kwa inu.

4. Tsono mithengayo inafika ku Gibeya kwa Sauli, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi.

5. Ndipo, onani, Sauli anacokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Sauli, Coliritsa anthu misozi nciani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabezi.

6. Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Sauli mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wace unayaka kwambiri.

7. Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthuli nthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israyeli, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Sauli ndi pa Samueli, adzatero nazo ng'ombe zace. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, naturuka ngati munthu mmodzi.

8. Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israyeli anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 11