3. Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Beteli, wina wonyamula ana a mbuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.
4. Iwowa adzakulankhulani, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m'manja mwao.
5. Ndipo m'tsogolo mwace mudzafika ku phiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumudziko mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi cisakasa, ndi lingaka, ndi toliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;
6. ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.
7. Ndipo zitakufikirani zizindikilo izi mudzacita monga mudzaona pocita, pakuti Mulungu ali nanu.