Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 1:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wace, ndi ana ace onse, amuna ndi akazi, gawo lao;

5. koma anapatsa Hana magawo awiri, cifukwa anakonda Hana, koma Mulungu anatseka mimba yace.

6. Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukuru, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yace.

7. Ndipo popeza munthuyo adatero caka ndi caka, popita mkaziyo ku nyumba ya Yehova, mnzaceyo amamputa; cifukwa cace iye analira misozi, nakana kudya.

8. Ndipo mwamuna wace Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? ndipo umakaniranji kudya? ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindiri wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?

9. Comweco Hana anauka atadya m'Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wace pa mphuthu ya Kacisi wa Yehova.

10. Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;

11. nalonjeza cowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukila ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wace, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pace.

12. Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pace.

13. Koma Hana ananena mu mtima; milomo yace inatukula, koma mau ace sanamveka; cifukwa cace Eli anamuyesa woledzera.

14. Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? cotsa vinyo wako.

15. Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndiri mkazi wa mtima wacisoni; sindinamwa vinyo kapena cakumwa cowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.

16. Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; cifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kucuruka kwa kudandaula kwanga ndi kubvutika kwanga.

17. Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israyeli akupatse copempha cako unacipempha, kwa iye.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 1