Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 25:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi ciwerengo ca anchito monga mwa kutumikira kwao ndko:

2. a ana a Asafu: Zakuri, ndi Yosefe, ndi Netaniya, ndi Asarela, ana a Asafu; mwa cilangizo ca Asafu, wakunenera mwa cilangizo ca mfumu.

3. A Yedntuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa cilangizo ca atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.

4. A Hemani, ana a Hemani: Bukiya, Mataniya, Uziyeli, Sebuyeli, ndi Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, ndi Romamti-Ezeri, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, Mahazioti;

5. awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m'mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yace. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana amuna khumi ndi anai, ndi ana akazi atatu.

6. Onsewa anawalangiza ndi atate wao ayimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 25