A Yedntuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa cilangizo ca atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.