Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Cigawo ca oyimbira nyimbo

1. Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi ciwerengo ca anchito monga mwa kutumikira kwao ndko:

2. a ana a Asafu: Zakuri, ndi Yosefe, ndi Netaniya, ndi Asarela, ana a Asafu; mwa cilangizo ca Asafu, wakunenera mwa cilangizo ca mfumu.

3. A Yedntuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa cilangizo ca atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.

4. A Hemani, ana a Hemani: Bukiya, Mataniya, Uziyeli, Sebuyeli, ndi Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, ndi Romamti-Ezeri, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, Mahazioti;

5. awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m'mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yace. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana amuna khumi ndi anai, ndi ana akazi atatu.

6. Onsewa anawalangiza ndi atate wao ayimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.

7. Ndipo ciwerengo cao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa ayimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.

8. Ndipo anacita maere pa udikiro wao, analingana onse, ang'ono ndi akuru, mphunzitsi ndi wophunzira.

9. Maere oyamba tsono anagwera a banja la Asafu ndiye Yosefe; waciwiri Gedaliya, iye ndi abale ace, ndi ana ace khumi ndi awiri;

10. wacitatu Zakuri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

11. wacinai Izri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

12. wacisanu Netaniya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

13. wacisanu ndi cimodzi Bukiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

14. wacisanu ndi ciwiri Yesarela: ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

15. wacisanu ndi citatu Yesaya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

16. wacisanu ndi cinai Mataniya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri:

17. wakhumi Simeyi, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

18. wakhumi ndi cimodzi Azareli, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

19. wakhumi ndi ciwiri Hasabiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

20. wakhumi ndi citatu Subaeli, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

21. wakhumi ndi cinai Matitiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

22. wakhumi ndi cisanu Yeremoti, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

23. wakhumi ndi cisanu ndi cimodzi Hananiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

24. wakhumi ndi cisanu ndi ciwiri Yosibekasa, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

25. wakhumi ndi cisanu ndi citatu Hanani, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

26. wakhumi ndi cisanu ndi cinai Maloti, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

27. wa makumi awiri Eliyata, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

28. wa makumi awiri ndi cimodzi Hotiri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

29. wa makumi awiri ndi ciwiri Gidaliti, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

30. wa makumi awiri ndi citatu Mahazioti, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;

31. wa makumi awiri ndi cinai RomamtiEzeri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri.