Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 19:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo zitatha izi, Nahasi mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndi mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

2. Ndipo Davide anati, Ndidzamcitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wace anandicitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wace. Pofika anyamata ace a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,

3. akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kucitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? sakudzerani kodi anyamata ace kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?

4. Ndipo Hanuni anatenga anyamata a Davide, nawameta, nadula malaya ao pakati kufikira m'matako, nawaleka acoke.

5. Pamenepo anamuka ena, namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anacita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndebvu zanu; zitamera mubwere.

6. Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente cikwi cimodzi a siliva, kudzilembera magareta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-maaka, ndi ku Zoba.

7. Momwemo anadzilembera magareta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ace; nadza iwo, namanga misasa cakuno ca Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 19