Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 9:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero cifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino?

9. Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adaturutsa makolo ao m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, nailambira, naitumikira; cifukwa cace Yehova anawagwetsera coipa conseci.

10. Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomo adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;

11. popeza Hiramu mfumu ya Turo adamthandiza Solomo ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golidi yemwe, monga momwe iye anafuniramo, cifukwa cace mfumu Solomo anampatsa Hiramu midzi makumi awiri m'dziko la Galileya.

12. Ndipo Hiramu anaturuka ku Turo kukaona midzi adampatsa Solomoyo, koma siinamkomera.

13. Nati, Midzi yino mwandipatsayi njotani, mbale wanga? Naicha dzina lao, Dziko lacikole, kufikira lero lino.

14. Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalenti a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri.

15. Ndipo cifukwa cace ca msonkho uja anausonkhetsa mfumu Solomo ndi cimeneci; kuti amange nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya iye yekha, ndi Milo, ndi linga la Yerusalemu, ndi Hazori, ndi Megido; ndi Gezeri.

16. Pakuti Farao mfumu ya Aigupto adakwera nalanda Gezeri, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mudzimo, naupereka kwaulere kwa mwana wace mkazi wa Solomo.

17. Ndipo Solomo anamanganso Gezeri, ndi Betihoroni wakunsi,

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 9