Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:63-66 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

63. Ndipo Solomo anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israyeli onse anapereka nyumbayo ya Yehova.

64. Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pace pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidacepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.

65. Ndipo nthawi yomweyo Solomo anacita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israyeli yense pamodzi naye, msonkhano waukuru wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Aigupto, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.

66. Tsiku lacisanu ndi citatu anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema ao osekera ndi okondwera mtima cifukwa ca zokoma zonse Yehova anacitira Davide mtumiki wace, ndi Israyeli anthu ace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8