Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:52-64 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

52. kuti maso anu akatsegukire pembedzero la kapolo wanu ndi pembedzero la anthu anu Aisrayeli, kuwamveram'menemonseakapfuula kwa Inu.

53. Popeza Inu munawapatula pa anthu onse a pa dziko lapansi akhale colowa canu, monga munanena ndi dzanja la Mose mtumiki wanu, pamene munaturutsa makolo athu m'Aigupto, Yehova Mulungu Inu.

54. Ndipo kunali kuti atatsiriza Solomo kupemphera kwa Yehova pemphero ndi pembedzero lino lonse, ananyamuka ku guwa la nsembe la Yehova pomwe analikugwada pa mabondo ace, ndi manja ace otambasulira kumwamba.

55. Naimirira, nadalitsa msonkhano wonse wa Israyeli ndi mau okweza, nati,

56. Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ace Aisrayeli, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayika mau amodzi a mau ace onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wace.

57. Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga umo anakhalira nao makolo athu, asatisiye kapena kutitaya;

58. kuti atitembenuzire kwa iye yekha mitima yathu iyende m'njira zace zonse, ndi kusunga malamulo ace onse ndi malemba ace ndi maweruzo ace, amene anawalamulira makolo athu.

59. Ndipo mau anga amenewa ndapembedzera nao pamaso pa Yehova akhale pafupi ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti alimbitse mlandu wa kapolo wace, ndi mlandu wa anthu ace Aisrayeli, mlandu wa tsiku pa tsiku lace;

60. kuti anthu onse a pa dziko lapansi akadziwe kuti Yehova ndiye Mulungu, palibe wina.

61. Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malemba ace ndi kusunga malamulo ace, monga lero lino.

62. Ndipo mfumu ndi anthu onse a Israyeli pamodzi naye anaphera nsembe pamaso pa Yehova.

63. Ndipo Solomo anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israyeli onse anapereka nyumbayo ya Yehova.

64. Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pace pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidacepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8