Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo akulu onse a Israyeli anadza, ansembe nanyamula likasa.

4. Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi cihema cokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'cihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.

5. Ndipo mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Israyeli wosonkhana kwa iye anali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, cifukwa ca unyinji wao.

6. Ndipo ansembe analonga likasa la cipangano ca Yehova kumalo kwace, ku monenera mwa nyumba, ku malo opatulikitsa, munsi mwa mapiko a akerubi,

7. Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zace.

8. Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika cakuno ca monenera; koma sizinaoneka kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.

9. Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja amwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israyeli, poturuka iwo m'dziko la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8