Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 5:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena coipa condigwera.

5. Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wacifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.

6. Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebano, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni.

7. Ndipo kunacitika, pamene Hiramu anamva mau ace a Solomo, anakondwera kwakukuru, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 5