Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 4:22-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo zakudya za Solomo zofikira tsiku limodzi zinalr miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete,

23. ng'ombe zonenepa khumi, ndi ng'ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta.

24. Pakuti analamulira dziko lonse liri tsidya lino la Firate, kuyambira ku Tipsa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya tino la Firate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko,

25. Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wace ndi mkuyu wace, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.

26. Ndipo Solomo anali nazo zipinda za akavalo a magareta ace zikwi makumi anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri.

27. Ndipo akapitao aja anatengetsera cakudya Solomo ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomo, munthu yense m'mwezi mwace, sanalola kanthu kasoweke.

28. Barelenso ndi udzu wa akavalo ndi ngamila anabwera nazo kumalo kwao, munthu yense monga momwe anamuuzira.

29. Ndipo Mulungu anampatsa Solomo nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa za mitundu mitundu, zonga mcenga uli m'mbali mwa nyanja.

30. Ndipo nzeru ya Solomo inaposa nzeru za anthu onse a kum'mawa, ndi nzeru zonse za ku Aigupto.

31. Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezra, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yace inafikira amitundu onse ozungulira.

32. Ndipo ananena miyambo zikwi zitatu, ndipo nyimbo zace zinali cikwi cimodzi mphambu zisanu.

33. Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebano kufikira hisopi wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.

34. Ndipo anafikako anthu a mitundu yonse kudzamva nzeru ya Solomo, ocokera kwa mafumu onse a dziko lonse lapansi, amene adamva mbiri ya nzeru yace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 4